KUPHA NYANI WA CHINASI

WOLEMBA

KAGWA OFC DZONZI

“Bambo  Chriss Samva mukuyenera kukagwira ntchito ya kalavula gaga kundende ya Chilili kwa zilumika khumi, basi mlandu wathera pompa.” Adatsendera chonchi ogamula mulanduyo, ukamuyang’anistitsa pakamwa pake amkaoneka kuti alibeso mawu ena aliwonse ndipo sangasintheso maganizo ngakhale ozengedwa mulanduwe utalira ngati khanda kuti ukhululukidwe. Nayeso Samva misonzi yosamba idayamba kunyowetsa gwanda lomwe adavala, mmaso mwake munkaoneka ng’anjo yakhwiyo ndi misonzi yosatonthozeka poganizira mulu wazaka zomwe akakhale akuseweza ntchito yakalavula gaga pa ku ndende ya Chilili amutumizako. Ali muunyolo choncho potuluka mukhothilo adafunitsitsa atadziwa dzina la munthu ozenga milandu uja, munthu amene kwa iye akadafunistitsa akadapanda kulengedwa poganizira zachilango chomwe adamupatsacho. Adauzidwa kuti kastwiri wozenga milanduyo adali Madalitso Botolo ndipo ndi mkulu wazamilandu watsopano pa khotilo. “ Oh mwati Kabotolo, oh? Chabwino” Adayankha modzidzimuka choncho Samva atauzidwa za dzina lamkulu amene amkafuna kumudziwayo. Dzinali  silimkaveka lachilendo kwaiyeyo ndipo samkakayikira kuti mwanjira iliyonse amkayenera kumudziwa mkuluyu basi. Atasinkhasinkha adatsimikizadi kuti ankamudziwa kastwiriyo, adali mkalasi imodzi pasukulu yapulaimale ya Olokani zaka zapitazo, Botolo adali mwana wa anthu wamba ndipo kwawo kudali kosauka koma adali mnyamata olimbikira sukulu mpaka kudzafika paudindo wapamwamba omwe Samva sanakhulupire atasowana kwa zaka zankhaninkhani. Samva masiku adzanawo adali mwana wa anthu anthu akumpanda kokhala agalu omva chingerezi koma sukulu adalibe nayo chidwi kupatulapo kumangochitira amzake matama kuti kwawo kuli chuma ndipo atapitaso kusekondale wake udali mowa ndi akazi omwe amkamuthandiza kudya ndalama zakwawozo ngati njenjete. Mphuno salota adakali kusekondale komko makolo ake onse adamwalira kusiya chuma chonse mmanja mwa Samva ndi alongo ake awiri pokuti iye ndiye adali chisamba m’bere mwawo. Apo mmalo mokumbulira malangizo amakolo kuti alimbikire sukulu adzagwire abale akewo pamkono patsogolo iye adaisiya sukuluyo kumangomwa mowa mpakana kumangogulista katundu, nyumba ndi galimoto zomwe makolowo adasiya ndipo abale akamudzudzula amkawauza kuti akhale chete zam’banja mwawo sizikuwakhudza. Chilichonse chimatha, palibe chosatha, chuma amkatukwanira anthucho chidawatsatira omwe adachipanga kumanda ndipo chifukwa choifunitsitsa ndalama komaso kusadziwa ntchito iliyonse Samva adayamba kumathyola nyumba zawanthu kumaba katundu wosiyanasiyana. Khalidweli litalowa mchala katakweyu adayamba kuyenda ndi mbava zina zokuba moopseza ndi mfuti ndipo tsiku lina adakathyola banki lina kuti abemo ndalama koma tsoka ndilo apolisi adawathothako ndipo amzake onse adakwanitsa kuthawa ogwidwa pagulupo adali iye yekha.Tsiku la mlandu litakwana apolisi adatengera kukhoti kuyankha mlandu okuba moopseza ndi mfuti, opezeka ndi mfuti mopanda chiloleza ndi ina ingapo. Nayeso ozenga mlanduyo sadaumire polanga chigandangachi ndi zilumika khumi kuti akachimine chobalalistira dzala pa katundu wa eni. Kunali kulira kwadzaoneni kuopa ntchito yakalavula gagayo koma wozenga mlanduyo sadakhululuke ndipo Samva adangoti diso ton’go ngati kalulu ali pachitsamba.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *