WABANJA SAMASOWA

WOLEMBA

KAGWA OFC DZONZI

Adali mayi wamsinkhu  wake  Brandina, akamayenda  kukongola kukumuwalitsa ngwethi ngwethi ngati zichitira ziphaniphani mumdima, adalidi nyali kwa awo odziwa kusankha nyenyezi kuti zikhale akazi awo. Mudera lonse la Mfumu Kwavuta akanathatu kupambana kutakhala komasankha nkhope za akazi owooneka mochitsa kaso, inde aja timati obadwa bwino! Chodabwitsa nthawi ndizilumika zimkapita popandapo nditambala mmodzi yemwe okaonekerako kwamakolo ake kuti mwina anthu ayimbeko nthungululu inde kumangidwa ukwati oyera. Amzake ambiri a Brandina anthanga imodzi adali kumutumizira mauthenga awukwati pafupifupi sabata liri lonse ndipo namwari adatopa ndikupita zikwati za eni, nayeso amkafuna anthu atavinako ukwati wake basi,  ngakhale ena amati kulibe manda ambeta koma kwa Brandina kufa mbeta kudali ngati kulephera kulowa ku paradizo. Nkhawa ndi chitonzo zitafikapo Brandina adafika pachisawawa pongopanga chibwenzi komaso kugona ndimwamuna aliyense bola ngati mamunayo wamuuza kuti amukwatira. Kunali kudziboda ndikusintha  zovala  mwana wamkazi kuti mwina mwamuna wabanjayo asokoloke pachithukuluzi chaubatchala alowe naye mmbanja ndipo mmene amalifunira banjalo ngakhale mwamuna atamufunsira lero mkumuuzaso kuti alowe mmbanjamo lero lomwe akanatha kulorela ndithu. Koto! Ikakuona litsilotu paja simasiya kuvumba, amuna onse omwe amakumana nawo Brandina adali ongofuna kumuvula basi, enaso amamubera ngakhale ndalama ndi katundu ndipo kwanthawi ina adapangapo chibwenzi ndimwamuna okwatira kale yemwe mkazi wake adamupitira pakhomo kukamumenya mpaka kumukomoka, adaziona mwana wamkazi chifukwa chofunafuna mwamuna wabanja.

Ataona kuti njira zonse sizikutheka adayamba kuyenda yenda mmatchalitchi atalangizidwa ndi mzake wina Martha kuti mmalo opemhpeleramo ndimo mukumapezeka mabanja mosavuta, ndiye kunali kuyenda mmakachisi mwana wamkazi  kuchita kukhala ngati Paulo mtumwi wakuDamasiko akugawa uthenga wabwino kuti mwina mwake ndikumpeza wakumalotoyo. Chokhumdwitsa namoso mmipingo amapita kumakanamizira kupempheramo amangokumanaso ndi amuna ake akapsari okhaokha kuti bolaso omwe amkamupusitsa achikunja aja adali bwino, kupusitsidwa ndimunthu yemwe amkamuona ngati opemphera kwa iye adali malodza adzuwa likuswa mtengo koma amkaiwala kuti ngakhaleso mmunda wa tirigu nansongole amathaso kupezeka mkumakula mosangalala. Chidamukhudwitsa kwambiri ndi ubwenzi umene adapanga ndi mneneri Tsokalawo wampingo wa ,’Miseche nenani mipingo kusiyana,’ ubwenziwu udayamba pamene mneneriyu adamuuza Brandina kuti Mulungu wamuonetsera kuti akhale mkazi wake tsiku loyamba lenileni lomwe mkaziyu adakapemphera nawo kumpingo kwaoko. Ngakhale amkalifunitsitsa banja mwana wa mkazi adayamba kufunsa mneneriyu mafunso kuti Mulunguyo wamuonetsera litilo pokuti iye ndi mneneriyo adali asadakumanepo chiyambire, “kodi Mulungu wakuonetsani kuti ine ndikhale mkazi wanuyo ndiye uti? Eeee koma inu apulofeti lero ndi lero mukanene kuti mwandikonda mukufuna timange banja koma mulungu wanuyo sanakunamizeni?” Adafunsa choncho podabwa ndizomwe yemwe anthu amkamutcha kuti mneneri wa Mlunguyo amkanena. “ Aaa kodi ukuyankhula ngati siiwe wamkulu muuzimu bwanji, inetu ndakhala ndikukwera mapiri, zulu, zigwa ndi madambo kupemphera kuti Mlungu andipatse mkazi ndipo adandionetsa kale iweyo tisanadziwane ndipo ndinakuona kale mu uzimu kuti lero ubwera.” Adatsimikiza choncho mneneri Tsokalawo uku akunyambitira milomo ngati wadya mang’ina anyani wachiyenda chokha kuyang’anitsitsa pankhope pa namwariyo kuti awone ngati mingoli yachikondi amkayimbayo imkalowadi mmaganizo achiphadzuwacho. Kuyamba kwa ubwenzi kunali komweko ndipo posakhalitsa asanayambeso ndidongosolo labanja Brandina adazindikira kuti adali ndi pathupi pa mneneriyo koma atamudziwitsa adakana kwamtu wa garu wachiwewe kuti iye simwini pathupipo, posakhalitsaso kudabukaso mbiri kuti mneneri Tsokalawo adali ataperekaso mimba kwa akazi ambiri kuderalo  kuphatikizapo akumpingo kwake. Nkhani idafika povuta ndipo anthu okwiya ndimchitidwe wa mneneriyo adakaotcha  kachisi ndi nyumba yomwe amakhala. Kuthawa kwa Tsokalawo mderali kudali komweko. Brandina atamva izi adangoti kakasi ngati nyau yazizidwa, Amusiyira pathupi, kodi mneneri wachimasomaso ngati ameneyu sadamusiireso matenda opatsirana pogonana mdzina lofunitsitsa mwamuna wabanja?

 

 

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *