Ukathyali wopandapake

Ukathyali wopandapake

“Tilandire nawo mpando wakumbuyowo mabwana ndi madona,ndimafuna nditoleretu zanga basi yathu isadawuyatse ulendo chifukwa ena mumachulutsa zodandaula tikanyamuka ndalama tisadatolere”,adalamula wothandizira dilayivala.

Iye adakhala ngati walota kuti panthawiyo ena mwa anthuwo adali akathyali womwe samafuna kulipira ponena kuti ndi abubu(wosalankhula) ngati njira imodzi yoti awamvetsetsere akapereka dandaulo lawo .

Pozindikira kuti ndalama zomwe amayenera kuyendera ulendo wawo wochoka ku Mzuzu kupita ku Dedza athera mowa komanso akazi osangalatsa anthu mmalo omwera mowa.Gwazani ndi mzake Gwirani pulani idawadzera mmalingaliro mwamsanga yoti athandizidwire poti iwo amayenera kuti zivute zitani anyamuke  ndithu ulendo wawo potengera mwambo wachiliza womwe udali kumudzi kwawo.Moti chilichonse chidali kudikila iwo poti ndi omwe amawoneka otchakukako nzeru pabanja lawo.

Atafika mdepoti ya Mzuzu adakweradi ‘basiyo ‘ ndipo iwo awiri adakhaladi chete monga momwe adagwirizirana akakwera.Ngakhale anthu adali kukambirani nkhani zosiyanasiyana zamsangulutso kaya zandale iwo samaseka nawo kapena kuyankhirapo popezeza akadati atero kukadakhala kunswa pangano lawo.Moti ana amuna adalimbadi mtima  osalankhula kapena kuyankhira chilichonse.ngkhle pkamwa pawo pamasonyeza kuti ali ndi mawu koma sizidatheke kutero moti anthu owona adawakhulupirira mosavuta.

Ndipo aliyense yemwe adali m’basimo  sadachite kuwuzidwa kuti akwera ndi anthu osalankhula chifukwa cha momwe amachezera awiriwo popeza amangolankhula ndi manja osatulutsa mawu .Adazindikira mwamsanga kuti adali ndi anthu avuto losankhula.itafika nthawi yoti ayambe kutolera chuma chake wothandizira basiyo,akamunawo adapereka zizindikiro zomwe zimasonyeza kuti alibe ndalama.koma nanga ndi ndani yemwe adakakamiza anthu achilemawo kuti alipirebe?akadawalamula kuti atsike kapena ?kutelokonso kukadakhala kuwalakwira potengera vuto lawo.Kenaka kondakitalayo adawamvetsetsa kuti asalipire.

Atafika mu Lilongwe dilayivala adathera pompo ndipo aliyense idali nthawi yake yoti atsike ndikufunanso mayendedwe ena maka kwa omwe ulendo wawo udali wopitilira kufika ku Blantyre.

Atakwera minibus Gwirani ndi Gwazani adachitanso chimodzimodzi ngati abubu.ndipo adamvetsetsedwanso.

Koma chidatsitsa dzaye chidali choti ,atawona kuti dilayivala akupyoletsa pa siteji yakwawo iwo adalephera kuwugwira mtima ndipo onse awiri adakuwa amvekera ,’adilayivala mukutipitilitsa potsikira’.Aliyense adagwira pakamwa mminibasimo ,powona kuti anthu omwe amati ndi osalankhula atulutsa mawu.

Izi zidakwiyitsa dilayivalayo komanso kondakitala ndipo mzachidziwikireni amayenera kuchitapo kanthu poti adadyetsedwa nyama ya galu ndi abambowo.

“Mesa inu mumati simumalankhula kumayambiririro awulendo uja,nde zakhala bwanji kuti mulankhule ?kapena ububu watha poti ndakupyoletsa siteji yakwanu?”adafunsa makwinya osonyeza ukali atamangana pa chipuni cha kondakitalayo.

Posakhalitsa adawawuza kuti alipire ndalama kupanda kutero adziwanso.Apa akamunawo adagwira njakata ndikusowa chonena poti mthumba mudalibe ngakhale 1 tambala. Ndipo  pomaliza adawufunsa kuti asankhe chimodzi kuwapatsa ndalamayo  kapena kuwaduduluzira kupolisi.

 

 [yop_poll id=”3″]

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *